Danzi lilibe mankhwala? Bodza. Anduna apita ku India kukachila ku Danzi

ku India kukachila ku Danzi
Danzi lilibe mankhwala?
Bodza. Anduna apita ku
India kukachila ku Danzi
Jan 05, 2021 Russell Kondowe
Health 0
A boma akuti anachoka mu dziko muno kuti
akapeze chithandizo pa vuto la mwendo lomwe
anali nalo. Eni ake akuti anakasaka chithandizo
pa Danzi lomwe likuwavuta koma ndalama zake
lalipila si boma. Mu zithunzi, ukuoneka ndi mutu
omangidwa ma bandechi osati mwendo ayi.
Nduna ya zamasewero a Ulemu Msungama
yadabwitsa a Malawi kutamveka ma lipoti oti ili
mu dziko la India kusakasaka chithandizo choti
ichile ku ‘matenda a danzi’.
Malinga ndi malipoti, a Msungama anachoka mu
dziko muno ma sabata awiri apitawo kupita ku
chipatala mu dziko la India. Nduna za boma
zinauza atolankhani kuti a Msungama
anatumizidwa ku chipatala ku India kuti
akapezeko chithandizo pa vuto la mwendo.
Zinatsimikiza kuti ulendo wawo unalipilidwa ndi
boma.
Koma chadabwitsa anthu ndi zithunzi zimene
zatuluka kuonetsa a Msungama ali ndi mutu wa
mu ma bandechi kusonyeza kuti chithandizo
chimene alandila ndi cha m’mutu.
Zithunzizi zapangitsa a Malawi kudabwa kuti
chomwe chinavuta a Msungama ndi chani
kwenikweni. Anthu ena ayambapo kunena kuti a
Msungama anapita mu dziko la India kuti
akabise Danzi lawo limene layamba kuonekela
mowala.
Koma a Msungama eni ati iwo anapita mu dziko
la Inida ndi vuto la mwendo ndipo ali kumeneko
anapezelapo mwayi oti achita opeleshoni
yobwenzeletsa tsitsi mmutu.
Malinga ndi malipoti a atolankhani, a Msungama
ati anawauza kuti boma silinalipile dongosolo
lothana ndi Danzi lawo ndipo mmalo mwake
lalipila ndi bungwe lothandiza anthu pa za umoyo
wawo la MASM.
“Boma langolipila za chithandizo cha mwendo
wanga, zakuthana ndi danzi langa alipila ndi a
bungwe la MASM,” akuti a Msungama anatelo.
Koma anthu odziwa momwe bungwe la MASM
limagwilila ntchito ati ndi kosatheka kuti
bungweli likalipile ndondomeko yobwenzeletsa
tsitsi kapena kuti yochilitsa munthu ku matenda
a Danzi.

Comment Here