Maji Yachita thiphwa Epsode 2

Maji Yachita thiphwa Epsode 2

Spread the love

Epsode 2

¶¶¶¶¶¶¶¶¶¶¶

Mu part 1 tinasiila pomwe Sammie anali atakanidwa ndipo mbiri yawanda.

Tipitilize

Tsiku linali lolemba pomwe Sammie anali akudzimvera chisoni chifukwa mbiri inali itawanda moipa.

Sammie atangolowa mkalasi oyamba kuyankhula anali Eliza.

Eeee koma amuna ena ngogwetsa ulesi mwamva inu..Hmmm…anayamba choncho Eliza.

Ndipo Jimmy sanachedwe kuyankha… Kodi Eliza ukuti bwanji?

Eeee adha anthu ena amachita kukhala ngati anatemera kukanidwa kodi sunamve?

*Kalasi yonse idaseka*

Iwe Eliza nde itiyo imeneyo?

Hahahahahaha Jimmy ukufuna uyidziwe?…Anthu muli pa k2 koma kumalota muli ndi k1000..mukungofuna kumatichulukitsila chiwerengero cha amuna omwe tawakanapo eti?…Amayankhula izi akuyang’ana komwe kunakhala Sammie.

Hahahahahaha iwe Eliza usamale adzakumenya anthu…

Hahahahahaha inu ma Swazi muzingoifinya…

*Kalasi yonse idaseka komatu Sammie amamva kuwawa mkati mwake.Maganizo otuluka amabwera koma amaopa.Mwamwayi aphunzitsi anabwera ndipo anali a life skills.ana aja anasiya Kaye ndipo sala aja anayamba kuphunzitsa.*

Today we want to learn about interpersonal relationships.Be open in this lesson.
Awa anali sir aja Mr Steven.
Osanama sir awa ntchito amayigwira ndipo ana amamva kukoma.Komatu tsikuli anqphunzitsa zosowa zija ndipo mkalasi munali zii.
Sir Steven anapeleka mwayi wamafunso.

Is there anyone with questions?

Apa Eliza anaimika mkono.

*Sir munakamba kuti one of the types of relationship is between males and females,ndekuti kumufunsila wina mkukukana zimakhala kuti ubale uwu suutheka eti?

*Atafunsa funsoli anthu anadumpha uku akukuwa ena akuomba ma desk kusonyesa kusangalala.*

*Sir Steven sanayankhe nsanga chifukwa zinawadabwitsa.atamwaza maso anaona kuti Sammie anali atazolika ndipo dir aja anayankha.Mayankhidwe ake anali achikulu chifukwa amakaikila china chake.Sammie anali wanzeru koma samanyada koma tsikuli chete wake anawadabwitsa sir aja koma anatuluka osafunsa kanthu.
Sir Steven atatuluka mpomwe kumalowa Sir Bern.Atangolowa ana onse anachita kunyadila chifukwa anali amolalo.Ana aja anaseka ndi momwe anavalira Sir Bern patsikuli.
Anavala trouser lalifupi mmusimu.Ndipo linali lothina.Anavala chishati chachikulu ndipo tsikuli anavala taye yaitali yofika maondo.Nsapato anavala yopendama.Komatu Sir Bern amatchena koopsa koma tsikuli kaya chinali chani sindudziwa. Pa sukulu Imeneyi ana amawayamikila kuti amadziwa kuvala.
Koma atangolowa mkalasi muja ana onse anagwa ndiphwete ndithu.
Sir Bern pofuna kuwayika ana aja mu game anafunsa funso lanthabwala amvekere..

*Kodi mukundiseka mmene ndavaliramu monga mtakufunsilani simupita?*

Ana kunali malikhweru,kuomba ma desk ena akuvina.

Sir Bern anadabwa sizimene amayembekezera.
⛱⛱⛱⛱⛱⛱

*Musatalikile chifukwa part 3 ilipo*

*Kodi inu mukanakhala Sammie mukanatani?*

*Team Wozi zur*

Leave a Reply