Maji yachita thiphwa Epsode 1

Maji yachita thiphwa Epsode 1

Spread the love

Episode 1

Hahahahahaha iwe Sammie taziyang’ane nde undiyang’ane then uganize statement yako wakambayo…are you serious?

Hannah please kulola kapena kundikana zili mmanja mwako.. koma chonde usandinyoze choncho..

Sammie wazinyozetsa wekha,unatani osakapeza ananyoni uko omwe mungafanane type…Nde undimvetse…pa school ponse pano olo mwana wa form 1 sangakulore.Mkazi amafuna mamuna oti atha kumamuthandiza.Iweyo ungathandize ndani?

Ndakumva Hannah koma ndinakukonda ndavomeleza kugonja..

Ine ndipo kaya ndi minyama.Dzuwa lindiwalire,mwezi undiwalire,Nyenyezi zindiwalire….nde mpaka ndiwe wemwe?..Hmmm zufunika kukasikusula mchere ndithu kuti ndichotse tsokali… iweyo sungandifunsile ine ndipo nditalikile ukununkha mkamwa.

Ndapita Hannah it’s ok.

*Mmene zimachitika izi anyamata omwe anali pafupi amangomvetsera.Ndipo anaseka pomwe Sammie amasuntha.Pagululi  panali mtsikana wina yemwe amkangomvetsera momwe amanyozedwera Sammie.Dzina lake anali Grace.Mtsikanayu anangokhala osayankha ndipo anyamata aja ananyoza mtundu onse.Anyamatawa anali Kelvin,Chimwemwe,Lesten ndi Bruno.Kelvin anali nchibwenzi ndi Eliza.koma enao analibe.Eliza anali form 3 limodzi ndi Sammie.Koma Kelvin anali form 4.Kelvin anamuuza Eliza za zomwe zinachitika zija chifukwa kunalibeko.*

++++++++++++++++++++++++++++++++

Eliza anali wamatama ndipo anali ndi anzake awiri omwe amayenda nawo.Mmodzi anali Hannah uja yemwe anali form 4.

Nkhani yakukanidwa kwa Sammie inawanda ngati ma gwaladi otchedwa mbaula ali paliponsewa.

Nkhani ija inachitika weekend koma Monday mkalasi munavuta.

*Tisanaone za mkalasi timudziwe Sammie*

Sammie anali mnyamata ofatsa ndipo anali osakonda akazi.Kwao kunali kolemera koopsa koma palibe amadziwa.Amavala zopanda Pake komanso olo makhalidwe ake palibe akanadziwa kuti kwao mkwandalama.Anabadwa yekha m’banja lakwao.Makolo ake amadabwa chifukwa anali mwana opanda matama.Anzake ocheza nao amaoneka opanda kanthu chifukwa amakonda kucheza ndi anthu omwe akuoneka otsalira pazinthu.

Pa school iyi atafika anakonda mtsikana uja Hannah.

Komatu chifukwa cha kudzibisa kuja palibe amadziwa kuti kwao mkolemera.

China chinali choti chibadwileni sanapangeko chibwenzi.Mwa njira ina anaona kuti kunali bwino apeze mkazi kuti apangane za tsogolo ndipo mtima wake unakonda Hannah.

*Tione Hannah*

Uyu anali mtsikana okongola molapitsa ndipo palibe mnyamata akanaona mkungosiya osasilira.

Wamfupi ndimamudziwa ine ndipo wamtali nde nanji,Komatu uyu anali ndi kansinkhu kapadera.Kathupi kovomera bwino zakudya Kali see!..Timawu tosasa bwino.Amati akavala uniform pokalowa mkalasi amazunguza mitu ya anyamata.Olo aphunzitsi amayamba ajejema maka Hannah akabwera mochedwa.Mkalasi mwao aphunzitsi a Bern anamuika kutsogolo dala chifukwa uniform ija imakwera mmwamba akakhala ndipo timiyendo towezuka bwino ngati carrot timakodola chilakolako cha zigizigi mpira opanda magolo.Nthawi zina Sir aja amatha kuthamanga Kaye kunyumba mkuwaitana akazao kuti anaona khoswe akulowa kuchipinda.Ndipo akatero amabwera pakatha mphindi zingapo.

*Koma kaya amakatani?*

Izi amakondana kupanga akaona myendo ya Hannah.

*Hannah anali wamatama ndipo palibe mnyamata amayelekeza kumuyandikila.Kwao kunali kosauka koma amaoneka bwino chifukwa mkulu wake anali Ku Jons.Komatu tsiku lina amafunsilidwa ndi mnyamata ooneka waumphawi koma anamunyoza koopsa.Uyu anali Sammie*

 ~Ndikhulupilira tawadziwa ndipo tipitilize~

*Nkhani inawanda mpaka Sammie kusowa mtendere*

Mu part 2 tiona mmene munalili mkalasi.

Pangani comment muone…

SIR BERN CREATIONS

Leave a Reply